Menu

MASALIMO 128

BIB

1 Odala ndi onse amene amaopa Yehova, amene amayenda mʼnjira zake. 2 Udzadya chipatso cha ntchito yako; madalitso ndi chuma zidzakhala zako. 3 Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka mʼkati mwa nyumba yako; ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi kuzungulira tebulo lako. 4 Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa amene amaopa Yehova. 5 Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni masiku onse a moyo wako; uwone zokoma za Yerusalemu, 6 ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako. Mtendere ukhale ndi Israeli.

Everything we make is available for free because of a generous community of supporters.

Donate