Menu

MASALIMO 127

BIB

1 Yehova akapanda kumanga nyumba, omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe. Yehova akapanda kulondera mzinda, mlonda akanangolondera pachabe. 2 Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawa ndi kusagona msanga madzulo, kuvutikira chakudya choti mudye, pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda. 3 Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova, ana ndi mphotho yochokera kwa Iye. 4 Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja mwa munthu wankhondo. 5 Wodala munthu amene motengera mivi mwake mwadzaza. Iwo sadzachititsidwa manyazi pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.

Everything we make is available for free because of a generous community of supporters.

Donate