Menu

MASALIMO 123

BIB

1 Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu amene mumakhala kumwamba. 2 Taonani, monga momwe maso a akapolo amayangʼana mʼdzanja la mbuye wawo, monga momwenso maso a mdzakazi amayangʼana mʼdzanja la dona wake, choncho maso athu ali kwa Yehova Mulungu wathu, mpaka atichitire chifundo. 3 Mutichitire chifundo, Inu Yehova mutichitire chifundo, pakuti tapirira chitonzo chachikulu. 4 Ife tapirira mnyozo wambiri kuchokera kwa anthu odzikuza, chitonzo chachikulu kuchokera kwa anthu onyada.

Everything we make is available for free because of a generous community of supporters.

Donate