Menu

MASALIMO 122

BIB

1 Ndinakondwera atandiwuza kuti, “Tiyeni ku nyumba ya Yehova." 2 Mapazi athu akuyima mʼzipata zako, Iwe Yerusalemu. 3 Yerusalemu anamangidwa ngati mzinda umene uli wothithikana pamodzi. 4 Kumeneko ndiye kumene kumapita mafuko, mafuko a Yehova, umboni wa kwa Israeli, kuti atamande dzina la Yehova. 5 Kumeneko anayikako mipando yaufumu yachiweruzo, mipando yaufumu ya nyumba ya Davide. 6 Pemphererani mtendere wa Yerusalemu: “Iwo amene amakukonda iwe zinthu ziwayendere bwino. 7 Mukhale mtendere mʼkati mwa makoma ako, ndipo mʼnyumba zako zaufumu mukhale chitetezo." 8 Chifukwa cha abale anga ndi abwenzi anga ndidzati, “Mtendere ukhale mʼkati mwako." 9 Chifukwa cha Nyumba ya Yehova Mulungu wathu, ndidzakufunira zabwino.

Everything we make is available for free because of a generous community of supporters.

Donate