Menu

MASALIMO 87

BIB

1 Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera; 2 Yehova amakonda zipata za Ziyoni kupambana malo onse okhalamo a Yakobo. 3 Za ulemerero wako zimakambidwa, Iwe mzinda wa Mulungu: Sela 4 “Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni pakati pa iwo amene amandidziwa. Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi, ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ “ 5 Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti, “Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye, ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo." 6 Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina: “Uyu anabadwira mʼZiyoni.” Sela 7 Oyimba ndi ovina omwe adzati, “Akasupe anga onse ali mwa iwe."

Everything we make is available for free because of a generous community of supporters.

Donate