Menu

MASALIMO 70

BIB

1 Fulumirani Mulungu kundipulumutsa; Yehova bwerani msanga kudzandithandiza. 2 Iwo amene akufunafuna moyo wanga achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa; onse amene akukhumba chiwonongeko changa abwezedwe mopanda ulemu. 3 Onse amene akunena kwa ine kuti, “Aha, aha,” abwerere chifukwa cha manyazi awo. 4 Koma onse amene akufunafuna Inu akondwere ndi kusangalala mwa Inu; iwo amene amakonda chipulumutso chanu nthawi zonse anene kuti, “Mulungu akuzike!" 5 Koma ine ndine wosauka ndi wosowa; bwerani msanga kwa ine Inu Mulungu. Inu ndinu thandizo langa ndi momboli wanga; Inu Yehova musachedwe.

Everything we make is available for free because of a generous community of supporters.

Donate