MASALIMO 60
BIB1 Inu Mulungu mwatikanatu ife, ndipo mwatiwonongera otiteteza. Inu mwatikwiyira, tsopano tibwezeretseni mwakale! 2 Inu mwagwedeza dziko ndipo mwalingʼamba, konzani mingʼalu yake pakuti ikugwedezeka kwambiri. 3 Inu mwaonetsa anthu anu nthawi za mavuto; inu mwatipatsa vinyo amene watichititsa kudzandira. 4 Koma kwa iwo amene amaopa Inu, Inu mwakweza mbendera kuti tisonkhanireko pothawa uta. 5 Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja, kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe. 6 Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika: “Mwakupambana ndidzagawa Sekemu ndipo ndidzayeza malire a chigwa cha Sukoti. 7 Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso; Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera, Yuda ndi ndodo yanga yaufumu 8 Mowabu ndi mbale yanga yosambira, pa Edomu ndidzaponyapo nsapato yanga, pa Filisitiya ndidzafuwula mwakupambana." 9 Adzandifikitse ndani ku mzinda wotetezedwa? Ndani adzanditsogolera ku Edomu? 10 Kodi si Inu Mulungu, Inu amene mwatikana ife ndipo simutuluka pamodzi ndi magulu athu ankhondo. 11 Tipatseni chithandizo kuti tilimbane ndi mdani wathu, pakuti thandizo lochokera kwa munthu ndi lopanda phindu. 12 Chifukwa cha Mulungu, ife tidzapeza chipambano ndipo tidzapondaponda adani athu.
