Menu

MASALIMO 6

BIB

1 Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu, kapena kundilanga mu ukali wanu. 2 Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka; Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu. 3 Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu. Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti? 4 Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse; pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. 5 Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira; Amakutamandani ndani ali ku manda? 6 Ine ndatopa ndi kubuwula; usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga; ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi. 7 Maso anga atupa chifukwa cha chisoni; akulephera kuona chifukwa cha adani anga. 8 Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa, pakuti Yehova wamva kulira kwanga. 9 Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo; Yehova walandira pemphero langa. 10 Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha; adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.

Everything we make is available for free because of a generous community of supporters.

Donate