Menu

MASALIMO 54

BIB

1 Pulumutseni Inu Mulungu, mwa dzina lanu; onetsani kuti ndine wosalakwa mwamphamvu yanu. 2 Imvani pemphero langa, Inu Mulungu mvetserani mawu a pakamwa panga. 3 Alendo akundithira nkhondo; anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga, anthu amene salabadira za Mulungu. 4 Zoonadi Mulungu ndi thandizo langa; Ambuye ndiye amene amandichirikiza ine. 5 Lolani kuti choyipa chifike pa iwo amene amandichita chipongwe; mwa kukhulupirika kwanu awonongeni. 6 Ine ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu; ndidzatamanda dzina lanu, Inu Yehova, pakuti ndi labwino. 7 Pakuti Iyeyo wandipulumutsa ku masautso anga onse, ndipo maso anga apenya kupambana kwa pa adani anga.

Everything we make is available for free because of a generous community of supporters.

Donate