Menu

MASALIMO 131

BIB

1 Inu Yehova, mtima wanga siwodzikuza, maso anga siwonyada; sinditengeteka mtima ndi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa. 2 Koma moyo wanga ndawutontholetsa ndi kuwukhalitsa chete ngati mwana amene amayi ake amuletsa kuyamwa, moyo wanga mʼkati mwanga uli ngati mwana amene amuletsa kuyamwa. 3 Yembekeza Yehova, iwe Israeli, kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Everything we make is available for free because of a generous community of supporters.

Donate