Menu

MASALIMO 13

BIB

1 Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale? Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu? 2 Ndidzalimbana ndi maganizo anga ndi kukhala ndi chisoni mu mtima mwanga tsiku lililonse mpaka liti? Mpaka liti adani anga adzandipambana? 3 Ndiyangʼaneni ndi kundiyankha, Inu Yehova Mulungu wanga. Walitsani maso anga kuti ndingafe; 4 mdani wanga adzati, “Ndamugonjetsa,” ndipo adani anga adzakondwera pamene ine ndagwa. 5 Koma ndikudalira chikondi chanu chosasinthika; mtima wanga umakondwera ndi chipulumutso chanu. 6 Ine ndidzayimbira Yehova pakuti wandichitira zokoma.

Everything we make is available for free because of a generous community of supporters.

Donate