Menu

MASALIMO 120

BIB

1 Ndimafuwulira kwa Yehova mʼmasautso anga, ndipo Iye amandiyankha. 2 Pulumutseni Yehova ku milomo yabodza, ndi kwa anthu achinyengo. 3 Kodi adzakuchitani chiyani, ndipo adzawonjezerapo zotani, inu anthu achinyengo? 4 Adzakulangani ndi mivi yakuthwa ya munthu wankhondo, ndi makala oyaka a mtengo wa tsanya. 5 Tsoka ine kuti ndimakhala ku Mesaki, kuti ndimakhala pakati pa matenti a ku Kedara! 6 Kwa nthawi yayitali ndakhala pakati pa iwo amene amadana ndi mtendere. 7 Ine ndine munthu wamtendere; koma ndikamayankhula, iwo amafuna nkhondo.

Everything we make is available for free because of a generous community of supporters.

Donate