Menu

NEHEMIYA 7

BIB

1 Khoma linamangidwa ndipo zitseko zinayikidwa. Pambuyo pake alonda a Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo ndiponso Alevi anasankhidwa. 2 Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena. 3 Ine ndinawawuza kuti, “Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo." 4 Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe. 5 Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo: 6 Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake. 7 Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana. Tsono chiwerengero cha anthu a ku Israeli chinali chotere: 8 Zidzukulu za Parosi2,172 9 Zidzukulu za Sefatiya372 10 Zidzukulu za Ara652 11 Zidzukulu za Pahati-Mowabu (kudzera mu mʼbado wa Yesuwa ndi Yowabu)2,818 12 Zidzukulu za Elamu1,254 13 Zidzukulu za Zatu845 14 Zidzukulu za Zakai760 15 Zidzukulu za Binuyi648 16 Zidzukulu za Bebai628 17 Zidzukulu za Azigadi2,322 18 Zidzukulu za Adonikamu667 19 Zidzukulu za Abigivai2,067 20 Zidzukulu za Adini655 21 Zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya)98 22 Zidzukulu za Hasumu328 23 Zidzukulu za Bezayi324 24 Zidzukulu za Harifu112 25 Zidzukulu za Gibiyoni95. 26 Anthu a ku Betelehemu ndi Netofa188 27 Anthu a ku Anatoti128 28 Anthu a ku Beti-Azimaveti42 29 Anthu a ku Kiriati Yeyarimu Kefira ndi Beeroti743 30 Anthu a ku Rama ndi Geba621 31 Anthu a ku Mikimasi122 32 Anthu a ku Beteli ndi Ai123 33 Anthu a ku Nebo winayo52 34 Ana a Elamu wina1,254 35 Zidzukulu za Harimu320 36 Zidzukulu za Yeriko345 37 Zidzukulu za Lodi, Hadidi ndi Ono721 38 Zidzukulu za Senaya3,930. 39 Ansembe anali awa: A banja la Yedaya (ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa)973 40 Zidzukulu za Imeri1,052 41 Zidzukulu za Pasi-Huri1,247 42 Zidzukulu za Harimu1,017. 43 Alevi anali awa: A banja la Yesuwa ndi Kadimieli, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya74. 44 Anthu oyimba: Zidzukulu za Asafu148. 45 Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu zaSalumu, Ateri, Talimoni, Hatita ndi Sobai138. 46 Anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu zaZiha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti, 47 Zidzukulu Kerosi, zidzukulu za Siya, zidzukulu za Padoni 48 Zidzukulu za Lebana za Hagaba, ndi za Salimayi, 49 Zidzukulu za Hanani, zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, 50 Zidzukulu za Reyaya, zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nehoda, 51 Zidzukulu za Gazamu, zidzukulu za Uza, zidzukulu za Paseya, 52 Zidzukulu za Besai, zidzukulu za Meunimu, zidzukulu za Nefusimu, 53 Zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri, 54 Zidzukulu za Baziliti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa, 55 Zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema 56 Zidzukulu za Neziya, ndi zidzukulu za Hatifa. 57 Zidzukulu za antchito a Solomoni: Zidzukulu zaSotai, zidzukulu za Sofereti, zidzukulu za Perida 58 zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli, 59 zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatiluzidzukulu za Pokereti-Hazebaimu ndi zidzukulu Amoni. 60 Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo392. 61 Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi. 62 Zidzukulu zaDelaya, zidzukulu za Tobiya ndi zidzukulu za Nekoda642. 63 Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa: zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo). 64 Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo. 65 Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu. 66 Chiwerengero chonse cha anthuwa chinali 42,360. 67 Kuwonjezera pamenepa panali antchito awo aamuna ndi aakazi 7,337 ndiponso anthu aamuna ndi aakazi oyimba nyimbo okwanira 245. 68 Panali akavalo 736, abulu angʼonoangʼono 245. 69 Ngamira zawo zinalipo 435 ndipo abulu analipo 6,720. 70 Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530. 71 Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250. 72 Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67. 73 Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo. Ezara Awerenga Malamulo Pofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo.

Everything we make is available for free because of a generous community of supporters.

Donate