Menu

YOSWA 12

BIB

1 Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa: 2 Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi. 3 Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga. 4 Ogi mfumu ya mzinda wa Basani, amene anali mmodzi mwa otsala mwa Arefaimu. Iye ankakhala ku Asiteroti ndi Ederi. 5 Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni. 6 Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo. 7 Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo. 8 Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa: 9 mfumu ya Yerikoimodzimfumu ya Ai (kufupi ndi Beteliimodzi 10 mfumu ya Yerusalemuimodzimfumu ya Hebroniimodzi 11 mfumu ya Yarimutiimodzimfumu ya Lakisiimodzi 12 mfumu ya Egiloniimodzimfumu ya Gezeriimodzi 13 mfumu ya Debriimodzimfumu ya Gederiimodzi 14 mfumu ya Horimaimodzimfumu ya Aradiimodzi 15 mfumu ya Libinaimodzimfumu ya Adulamuimodzi 16 mfumu ya Makedaimodzimfumu ya Beteliimodzi 17 mfumu ya Tapuwaimodzimfumu ya Heferiimodzi 18 mfumu ya Afekiimodzimfumu ya Lasaroniimodzi 19 mfumu ya Madoniimodzimfumu ya Hazoriimodzi 20 mfumu ya Simuroni Meroniimodzimfumu ya Akisafuimodzi 21 mfumu ya Taanakiimodzimfumu ya Megidoimodzi 22 mfumu ya Kadesiimodzimfumu ya Yokineamu ku Karimeliimodzi 23 mfumu ya Dori ku Nafoti Doriimodzimfumu ya Goyini ku Giligalaimodzi 24 mfumu ya Tirizaimodzimafumu onse pamodzi analipo 31.

Everything we make is available for free because of a generous community of supporters.

Donate