EZARA 2
BIB1 Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake. 2 Iwo anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Seruya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana). Chiwerengero cha anthu aamuna a Israeli chinali chotere: 3 Zidzukulu za Parosi2,172 4 zidzukulu za Sefatiya372 5 zidzukulu za Ara775 6 zidzukulu za Pahati-Mowabu (zochokera kwa Yesuwa ndi Yowabu)2,812 7 zidzukulu za Elamu1,254 8 zidzukulu za Zatu945 9 zidzukulu za Zakai760 10 zidzukulu za Bani642 11 zidzukulu za Bebai623 12 zidzukulu za Azigadi1,222 13 zidzukulu za Adonikamu666 14 zidzukulu za Bigivai2,056 15 zidzukulu za Adini454 16 zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya)98 17 zidzukulu za Bezayi323 18 zidzukulu za Yora112 19 zidzukulu za Hasumu223 20 zidzukulu za Gibari95. 21 Anthu a ku Betelehemu123 22 Anthu aamuna a ku Netofa56 23 Anthu aamuna a ku Anatoti128 24 Anthu aamuna a ku Azimaveti42 25 Anthu aamuna a ku Kiriati Yearimu, Kefira ndi Beeroti743 26 Anthu aamuna a ku Rama ndi Geba621 27 Anthu aamuna a ku Mikimasi122 28 Anthu aamuna a ku Beteli ndi Ai223 29 Anthu aamuna a ku Nebo52 30 Anthu aamuna a ku Magaibisi156 31 Anthu aamuna a ku Elamu wina1,254 32 Anthu aamuna a ku Harimu320 33 Anthu aamuna a ku Lodi, Hadidi ndi Ono725 34 Anthu aamuna a ku Yeriko345 35 Anthu aamuna a ku Sena3,630. 36 Ansembe anali awa: Zidzukulu za Yedaya (kudzera mu banja la Yesuwa)973 37 Zidzukulu za Imeri1,052 38 Zidzukulu za Pasuri1,247 39 Zidzukulu za Harimu1,017. 40 Alevi anali awa: Zidzukulu za Yesuwa ndi Kadimieli (kudzera mwa ana a Hodaviya)74. 41 Anthu oyimba nyimbo anali awa: Zidzukulu za Asafu128. 42 Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za Salumu, zidzukulu za Ateri, zidzukulu za Talimoni, zidzukulu za Akubu, zidzukulu za Hatita ndi zidzukulu za Sobai139. 43 Otumikira ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu zaZiha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti, 44 zidzukulu za Kerosi, zidzukulu za Siyaha, Padoni, 45 zidzukulu za Lebana, zidzukulu za Hagaba, zidzukulu za Akubu, 46 zidzukulu za Hagabu, zidzukulu za Salimayi, zidzukulu za Hanani, 47 zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, zidzukulu za Reaya, 48 zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nekoda, zidzukulu za Gazamu, 49 zidzukulu za Uza, zidzukulu za Peseya, zidzukulu za Besai, 50 zidzukulu za Asina, zidzukulu za Meunimu, Nefusimu, 51 zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri, 52 zidzukulu za Baziruti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa, 53 zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema, 54 zidzukulu za Neziya ndi zidzukulu za Hatifa. 55 Zidzukulu za antchito a Solomoni zinali izi: Zidzukulu zaSotai, zidzukulu za Hasofereti, zidzukulu za Peruda, 56 zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli, 57 zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu,zidzukulu za Pokereti, Hazebayimu ndi Ami. 58 Chiwerengero cha onse otumikira ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za Solomoni chinali392. 59 Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi: 60 Zidzukulu za Delaya, zidzukulu za Tobiya, ndi zidzukulu za Nekoda. Onse pamodzi anali652. 61 Ndi ena pakati pa ansembe anali awa: Zidzukulu zaHobiya, Hakozi, ndi Barizilai (Zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai. Barizilai ameneyu ndi uja anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi ndipo ankadziwika ndi dzina la bambo wawoyo.) 62 Amenewa anafufuza mayina awo mʼbuku lofotokoza mbiri ya mafuko awo, koma mayinawo sanawapezemo, choncho anawachotsa pa unsembe ngati anthu odetsedwa pa zachipembedzo. 63 Bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo mpaka atapezeka wansembe wodziwa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu. 64 Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 42,360, 65 kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito awo aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Analinso ndi amuna ndi akazi oyimba nyimbo okwanira 200. 66 Anali ndi akavalo 736, nyulu 245, 67 ngamira 435 ndi abulu 6,720. 68 Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale. 69 Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100. 70 Ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmidzi ya makolo awo.
